Genesis 43:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe ataona Benjamini, adauza wantchito woyang'anira zonse panyumba pake kuti, “Anthu aŵa aloŵetse m'nyumba. Ndipo uphe nyama ndi kuiphika bwino, chifukwa anthu ameneŵa adya ndi ine masana ano.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Yosefe anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wake, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakonzere, chifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe ataona Benjamini ali pamodzi ndi abale ake, anati kwa wantchito wa mʼnyumba mwake, “Atengereni anthu awa ku nyumba kwanga, ndipo uphe nyama ndi kukonza bwino chakudya popeza amenewa adya ndi ine masana ano.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wace, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakoozere, cifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno.