Genesis 43:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iwowo adachita mantha kwambiri poona kuti akupita nawo kunyumba kwa Yosefeyo: ankaganiza kuti, “Akutiloŵetsa muno chifukwa cha ndalama zija zidabwezedwa m'matumba mwathu pa nthaŵi yoyamba ija. Akungofuna danga loti achite nafe nkhondo mwadzidzidzi, chifukwa akufuna kutisandutsa akapolo ake ndi kutilanda abulu athuŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthuwo ndipo anaopa, chifukwa analowezedwa m'nyumba ya Yosefe; nati, Chifukwa cha ndalama zija zinabwezedwa m'matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone chifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi abulu athu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anthu aja anachita mantha ataona kuti akuwatengera ku nyumba kwa Yosefe. Mʼmaganizo awo ankanena kuti, “Atibweretsa kuno chifukwa cha ndalama zija zinabwezeredwa mʼmatumba athu poyamba paja. Ameneyu akufuna kuti atipanikize ndi kutigwira ukapolo natilanda abulu athu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthuwo ndipo anaopa, cifukwa analowezedwa m'nyumba ya Yosefe; nati, Cifukwa ca ndalama zila zinabwezedwa m'matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone cifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi aburu athu.