Genesis 43:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Titafika pa malo a chigono, pomasula matumba athu, aliyense mwa ife adapeza ndalama zake kukamwa kwa thumba lake, ndipo ndalamazo zinalipo zonse monga momwe tidaaŵerengera. Ndalama zimenezo tabwera nazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma titafika pa malo ena kuti tigone, tinatsekula matumba athu ndipo aliyense wa ife anapeza ndalama zake momwe zinalili zili pakamwa pa thumba lake. Ndiye tabwerera nazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo panali pamene ife tinafika padgono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lace, ndalama zathu mkulemera kwace; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu.