Genesis 43:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo tabwera nazonso ndalama zina zodzagulira chakudya china. Amene adaika ndalama m'matumba mwathu, sitikumudziŵa ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndalama zina tatenga m'manja mwathu kuti tigule chakudya: sitimdziwa amene anaika ndalama zathu m'matumba athu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tabweretsanso ndalama zina kuti tigule chakudya. Sitikudziwa kuti kaya ndani anayika ndalamazo mʼmatumba athu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndalama zina tatenga m'manja mwathu kuti tigule cakudya: sitimdziwa amene anaika ndalama zathu m'matumba athu.