Genesis 43:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe atabwera, abale akewo adapereka mphatso zija kwa iye, ndipo adamuweramira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Yosefe anadza kunyumba kwake, analowa nazo m'nyumba mphatso zinali m'manja mwao, namweramira iye pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe atafika ku nyumbako, iwo anapereka mphatso zija namuweramira pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Yosefe anadza kunyumba kwace, analowa nazo m'nyumba mphatso zinali m'manja mwao, namweramira iye pansi.