Genesis 43:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe ataona Benjamini, mng'ono wake weniweni uja, adati “Uyu ayenera kukhala mng'ono wanu wotsiriza uja munkandiwuzayu. Mulungu akudalitse, mwana wanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anatukula maso ake naona Benjamini mphwake, mwana wa amake, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akuchitire iwe ufulu, mwana wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pomwazamwaza maso Yosefe anaona Benjamini, mʼbale wake weniweni wa bere limodzi, ndipo anafunsa, “Kodi uyu ndiye mʼbale wanu wamngʼono kwambiri amene munkandiwuza uja?” Kenaka anati, “Ambuye akukomere mtima mwana wanga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anatucula maso ace naona Benjamini mphwace, mwana wa amace, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akucitire we ufulu, mwana wanga.