Genesis 43:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yuda adati, “Munthu uja adatichenjeza kolimba kuti sadzatilola kuwonekera pamaso pake, tikapanda kupita naye mng'ono wathuyu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yuda anati kwa iye, “Munthu uja anatichenjeza monenetsa kuti, ‘Simudzandionanso ine pokhapokha mutabwera ndi mngʼono wanu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, Simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.