Genesis 43:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atanena zimenezo Yosefe adachokapo mofulumira chifukwa choti mtima wake udaadzaza ndi chifundo chifukwa cha mng'ono wake uja. Anali pafupifupi kulira, motero adapita m'chipinda mwake nakalirira m'menemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yosefe ndipo anafulumira, chifukwa mtima wake unakhumbitsa mphwake, ndipo anafuna polirira; nalowa m'chipinda chake naliramo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yosefe anafulumira kutuluka chifukwa mtima wake unadzaza ndi chifundo cha mngʼono wake ndipo anafuna kulira. Tsono anakalowa mʼchipinda chakechake nakalira kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anafulumira, cifukwa mtima wace unakhumbitsa mphwace, ndipo mafuna polirira; nalowa m'cipinda ace naliramo.