Genesis 43:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe ankadyera payekha, abale akewo ankadyera pa tebulo lina. Aejipito amene anali naye m'nyumba nawonso ankadyera paokha, chifukwa iwo ankanyansidwa kudyera pamodzi ndi Ahebri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuikira iye chake pa yekha, ndi iwo chao pa okha, ndi Aejipito akudya naye chao pa okha; chifukwa Aejipito sanathei kudya chakudya pamodzi ndi Ahebri: chifukwa kuchita chomwecho nkunyansira Aejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anamupatsira Yosefe chakudya payekha, abale ake aja pawokha, ndiponso Aigupto amene ankadya pamodzi ndi iye nawonso pawokha. Izi zinali choncho chifukwa Aigupto ankanyansidwa kudya pamodzi ndi Ahebri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuikira iye cace pa yekha, ndi wo cao pa okha, ndi Aaigupto ikudya naye cao pa okha; cifukwa aigupto sanathei kudya cakudya pamodzi ndi Ahebri: cifukwa kucita comweco nkunyansira Aaigupto.