Genesis 43:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abalewo adaakhala pa tebulo patsogolo pa Yosefe, ndipo anali ataŵaika motsatana ndi kubadwa kwao, kuyambira wamkulu mpaka wamng'ono. Abale aja ataona m'mene aŵakhazikira, adadabwa kwambiri namapenyetsetsana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anakhala pamaso pake, woyamba monga ukulu wake, ndi wamng'ono monga ung'ono wake; ndipo anazizwa wina ndi wina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale aja anawakhazika patsogolo pa Yosefe. Iwo anawakhazika monga mwa mabadwidwe awo kuyambira woyamba kubadwa mpaka wotsirizira; ndipo ankangoyangʼanitsitsana modabwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anakhala pamaso pace, woyanba monga ukuru wace, ndi wanng'ono mensa ung'ono wace; ndipo mazizwa wina ndi wina.