Genesis 43:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chakudya chomwe ankadyacho chinkachokera patebulo pa Yosefe, koma chakudya chopatsa Benjamini chinkaposa cha onsewo kasanu. Motero onsewo adadya ndi kumwa pamodzi ndi Yosefe mpaka kukhuta, ndipo adasangalala pamodzi naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anawagawira mitanda ya patsogolo pake; koma mtanda wa Benjamini unaposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ankawagawira chakudya kuchokera pa tebulo la Yosefe. Koma chakudya cha Benjamini chinkaposa cha ena onsewa kasanu. Motero anadya ndi kumwa mpaka kukhuta, ndipo anasangalala pamodzi ndi Yosefe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mawagawira mitanda ya patsogolo pace; koma mtanda wa Benjamini maposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye.