Genesis 43:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukapanda kulola, ife sitipita, popeza kuti munthu ameneyo adaneneratu kuti, ‘Sindidzakulolani kufika pamaso panga mukapanda kubwera naye mbale wanuyo.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mukapanda kumulola, ife sitipita, chifukwa munthuyo anatiwuza kuti, ‘Simudzandionanso pokhapokha mutabwera ndi mngʼono wanuyo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu.