Genesis 43:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Israele adati, “Chifukwa chiyani mudathinitsa zinthu pa ine pomuuza kuti muli ndi mbale wanu winanso?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Israele anati, Chifukwa ninji munandichitira ine choipa chotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Israeli anafunsa kuti, “Bwanji inu munandiputira mavuto oterewa pomuwuza munthuyo kuti muli ndi mʼbale wanu wina?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Israyeli anati, Cifukwa ninji munandicitira ine coipa cotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu?