Genesis 43:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adayankha kuti, “Ndiye kuti munthuyo ankangofunsitsa za ife ndi za banja lathu nkumati, ‘Kodi bambo wanu akali moyo? Kodi muli naye mbale wanu wina?’ Tsono ife tidaayenera kuyankha mafunso onseŵa. Nanga ife tikadadziŵa bwanji kuti iye atiwuza zoti mbale wathuyo tipite naye limodzi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? Ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anayankha, “Munthuyo ankangofunsafunsa za ife ndi za banja lathu. Iye anatifunsa kuti, ‘Kodi abambo anu akanali ndi moyo? Kodi muli ndi mʼbale wanu wina?’ Ife tinkangoyankha mafunso ake. Ife tikanadziwa bwanji kuti adzanena kuti, ‘Mubwere naye kuno mʼbale wanu’?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?