Genesis 43:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yuda adauza bambo wake Israele kuti, “Mnyamatayu patsani ine, ndipo tikonzeke kuti tinyamuke tizipita. Motero tonsefe, inuyo, ana athu pamodzi ndi ife, sitidzafa ndi njala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yuda anati kwa atate wake Israele, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yuda anati kwa Israeli abambo ake, “Muloleni mnyamatayo apite ndi ine, ndipo tinyamuka nthawi yomweyo, kuti ife ndi inu pamodzi ndi ana athu tikhale ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yuda anati kwa atate wace Israyeli, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.