Genesis 44:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Yosefe adalamula wantchito wamkulu woyang'anira nyumba yake kuti, “Dzaza matumba a anthuŵa ndi chakudya chambiri momwe angathe kusenzera. Ndipo ndalama za aliyense uziike pakamwa pa thumba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wake kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi chakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Yosefe analamulira wantchito wa mʼnyumba mwake kuti, “Adzazire chakudya anthuwa mʼmatumba mwawo monga mmene anganyamulire, ndipo uwayikire ndalama zawo pakamwa pa matumba awowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wace kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi cakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lace.