Genesis 44:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo wantchitoyo adati, “Chabwino. Komatu wina pakati panupa akapezeka ndi chikhocho, ameneyo akhala kapolo wanga, ena nonsenu muzipita mwaufulu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anati, Tsononso chikhale monga mwa mau anu: iye amene ampeza nacho adzakhala kapolo wanga; ndipo inu mudzakhala opanda chifukwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Chabwino, tsono zikhale monga mwaneneramu. Komatu aliyense amene angapezeke nacho chikhocho adzakhala kapolo wanga, ndipo ena nonsenu muzipita mwaufulu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye mati, Tsononso cikhale monga mwa nau anu: iye amene ampeza naco adzakhala kapolo wanga; ndipo inu nudzakhala opanda cifukwa.