Genesis 44:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wantchito wa Yosefe uja adafunafuna mosamala kwambiri kuyambira pa wamkulu mpaka pa wamng'ono, ndipo chikhocho adachipeza m'thumba la Benjamini.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anafunafuna kuyambira pa wamkulu naleka pa wamng'ono nachipeza chikho m'thumba la Benjamini:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anayamba kufufuza, kuyambira pa wamkulu mpaka pa wamngʼono. Ndipo chikhocho chinapezeka mʼthumba mwa Benjamini.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anafunauna kuyambira pa wamkuru naleka pa wamng'ono; nacipeza cikho n'thumba la Benjamini: