Genesis 44:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Yuda adati, “Kodi ife tinganene chiyani kwa inu, bwana? Tilinso ndi mau ngati? Tingathe kudziyeretsa bwanji? Mulungu waulula cholakwa chathu, bwana. Tonsefe bwana, ndife akapolo anu, osati mmodzi yekha amene wapezeka ndi chikhoyu ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yuda anati, Kodi tidzati bwanji kwa mbuyanga? Kodi tidzanenanji? Kapena tidzawiringula ife bwanji? Mulungu wapeza mphulupulu ya akapolo anu; taonani, tili akapolo a mbuyanga, ife ndi iye amene anampeza nacho chikho m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yuda anayankha, “Kodi tinganenenji kwa mbuye wanga? Tinena chiyani? Tingadzilungamitse bwanji? Mulungu waulula kulakwa kwa antchito anu. Ndipo tsopano ndife akapolo a mbuye wanga, ife tonse pamodzi ndi amene wapezeka ndi chikhocho.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndico Yuda anati, Kodi tidzati bwanji kwa mbuyanga? kodi tidzanenanji? kapena tidzawiringula ife bwanji? Mulungu wapeza mphulupulu ya akapolo anu; taonani, tiri akapolo a mbuyanga, ife ndi iye amene anampeza naco cikho m'dzanja lace.