Genesis 44:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yosefe adati, “Iyai! Ine sindingathe kuchita zotero. Yekhayo amene wapezeka ndi chikho, ndiye adzakhala kapolo wanga. Enanu mungathe kumabwerera kwanu kwa bambo wanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anati, Ngati kutheka kuti ndichite chotero! Munthu amene anampeza nacho m'dzanja lake adzakhala kapolo wanga: koma inu, kazipitani ndi mtendere kwa atate wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yosefe anati, “Sindingachite choncho ayi! Yekhayo amene wapezeka ndi chikhocho ndi amene akhale kapolo wanga. Ena nonsenu, bwererani kwa abambo anu mu mtendere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anati, Ngati kutheka kuti ndicite cotero! Munthu amene anampeza naco m'dzanja lace adzakhala kapolo wanga: koma inu, kazipitani ndi mtendere kwa atate wanu.