Genesis 44:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ife tidaakuyankhani kuti, ‘Tili naye bambo wathu wokalamba ndi mbale wathu wina wamng'ono amene adabadwa bambo wathuyo atakalamba kale. Mkulu wake wa mnyamata ameneyo adamwalira kale. Choncho m'mimba mwa mai wake, yekhayu ndiye amene ali moyo, ndipo bambo wake amamkonda kwabasi.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tili ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng'ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ife tinayankha, ‘Inde mbuye wathu, ife tili ndi abambo athu wokalamba, ndipo pali mwana wamwamuna wamngʼono amene anabadwa abambo athu atakalamba kale. Mʼbale wake anafa ndipo ndi yekhayo mʼmimba mwa amayi ake amene watsala ndipo abambo ake amamukonda.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tiri ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wace wamng'ono; mbale wace wafa, ndipo iye yekha watsala wa amace, ndipo atate wace amkonda iye.