Genesis 44:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ife tidamuuza bambo wathu kuti, ‘Sitingathe kupita popeza kuti munthu uja sakatilola kufika pamaso pake, tikapanda kupita ndi mng'ono wathuyu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ife tinati, Sitingathe kupita; mphwathu wamng'ono akakhala ndi ife, pamenepo tidzapita; pakuti sitingaone nkhope ya munthu uja, mphwathu wamng'ono akapanda kukhala ndi ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tinati, ‘Sitingathe kupitanso. Sitingapite pokhapokha mngʼono wathuyu apite nafe chifukwa munthu uja anati sitingaonane naye ngati mngʼono wathuyu sakhala nafe.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ife tinati, Sitingathe kupita; mphwathu wamng'ono akakhala ndi ife, pamenepo tidzapita; pakuti sitingaone nkhope ya munthu uja, mphwathu wamng'ono akapanda kukhala ndi ife.