Genesis 44:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
akakangoona kuti iyeyu palibe, basitu akafa. Ndiye kuti ifeyo ndi amene tidzachititse bambo wathu chisoni chofa nacho mu ukalamba wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kudzakhala pakuona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi chisoni imvi za atate wathu kumanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo akakaona kuti mnyamatayu palibe, basi akafa. Ife tidzakhala ngati takankhira abambo athu ku manda ndi chisoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kudzakhala pakuona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi cisoni imvi za atate wathu kumanda.