Genesis 44:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiponsotu bwana, ine ndidapereka moyo wanga kwa bambo wanga chifukwa cha mnyamata ameneyu. Ndidamuuza kuti ngati mnyamatayu sindidzabwerera naye, ndidzakhala wolakwa pamaso pa bambo wanga moyo wanga onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kapolo wanu anadziyesa chikole cha mnyamata pa atate wanga, kuti, Ndikapanda kumbwezeranso kwa inu, pamenepo ndidzakhala ndi chifukwa kwa atate wanga nthawi zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiponsotu ine ndinadzipereka kwa abambo anga kukhala chikole chotsimikiza kuti mnyamatayu ndidzamuteteza, ndipo ndinati, ‘Ngati sindibwerera naye mnyamatayu kwa inu, ndiye kuti ndidzakhala wochimwira inu abambo anga moyo wanga wonse.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kapolo wanu anadziyesa cikole ca mnyamata pa atate wanga, kuti, Ndikapanda kumbwezeranso kwa inu, pamenepo ndidzakhala ndi cifukwa kwa atate wanga nthawi zonse.