Genesis 44:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atangoyenda pang'ono kuchoka mumzindamo, Yosefe adauza wantchito wake wamkulu uja kuti, “Nyamuka, uthamangire anthu aja. Ukaŵapeza, uŵafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoipa kwa zabwino?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atatuluka m'mudzi asanamuke patali, Yosefe anati kwa tsanyumba wake, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Chifukwa chanji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atangotuluka mu mzinda muja, koma asanapite patali, Yosefe anati kwa wantchito wake, “Nyamuka atsatire anthu aja msanga. Ndipo ukawapeza, uwafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoyipa ndi zabwino?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ataturuka m'mudzi asanamuke patari, Yosefe anati kwa tsanyumba wace, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Cifukwa canji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino?