Genesis 44:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu nomwe mudaona kuti ife pochoka ku Kanani, tidabwera ndi ndalama zimene tidaazipeza m'matumba mwathu. Nanga tingaberenji siliva kapena golide m'nyumba mwa bwana wanu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, ndalama zija, tinazipeza kukamwa kwa matumba athu, tinazibwezanso kwa inu kutuluka m'dziko la Kanani; nanga bwanji tingabe m'nyumba ya mbuyanga kapena siliva kapena golide?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paja ife pobwera kuchokera ku Kanaani tinatenga ndalama kubwezera zimene tinazipeza mʼmatumba mwathu. Ndiye pali chifukwa chanji kuti tikabe siliva kapena golide mʼnyumba mwa mbuye wanu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ndalama zija, tinazipeza kukamwa kwa matumba athu, tinazibwezanso kwa inu kuturuka m'dziko la Kanani; nanga bwanji tingabe m'nyumba ya mbuyanga kapena siliva kapena golidi?