Genesis 45:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Yosefe sadathenso kudzigwira pamaso pa onse omtumikira aja. Adanena mokweza mau kuti, “Onse atuluke muno.” Motero panalibe ndi mmodzi yemwe wotsalira pamene Yosefe ankadziwulula kwa abale ake aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe sanakhoze kudziletsa pamaso pa onse amene anaima naye: nati, Tulutsa anthu onse pamaso panga. Ndipo panalibe munthu pamodzi ndi iye pamene Yosefe anadziululira yekha kwa abale ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yosefe sanathenso kuwugwira mtima kuti asalire pamaso pa antchito ake ndipo anafuwula kuti, “Aliyense achoke pamaso panga!” Motero panalibe wina aliyense pamene Yosefe anadziwulula kwa abale ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe sanakhoza kudziletsa pamaso pa onse amene anaima naye: nati, Turutsa anthu onse pamaso panga. Ndipo panalibe munthu pamodzi ndi iye pamene Yosefe anadziululira yekha kwa abale ace.