Genesis 45:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mungathe kudzakhala kuno ku dziko la Goseni, kuti mukhale pafupi ndi ine. Mudzakhale kuno inuyo, ana anu, zidzukulu zanu, nkhosa zanu ndi mbuzi zomwe, ng'ombe zanu pamodzi ndi zonse zimene muli nazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudzakhala m'dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo inu, ana anu, zidzukulu zanu, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe zanu ndi antchito anu amene muli nawo muzidzakhala mʼdziko la Goseni pafupi ndi ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudzakhala m'dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo;