Genesis 45:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukadzakhala ku Goseni, ine ndizidzakusamalani. Zaka za njala zikalipobe zisanu. Sindifuna kuti inu musauke pamodzi ndi banja lanu, ndi onse amene muli nawo.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzachereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndizidzakupatsani zakudya kumeneko chifukwa zaka zisanu za njala zikubwera ndithu. Kupanda kutero, inu ndi mabanja anu pamodzi ndi anthu anu onse mudzasowa chakudya.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzacereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nao.