Genesis 45:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muuzeni bambo wanga kuti ndili pa ulemerero waukulu ku Ejipito kuno. Mukamuuzenso bambo wanga zonse zimene mwaonazi ndipo fulumirani, mubwere naye kuno.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse m'Ejipito, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukawawuze abambo anga kuti ndili pa ulemerero ku dziko la Igupto kuno ndi zonse zimene mwaziona. Tsopano fulumirani kuti mukabwere nawo kuno abambo anga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse m'Aigupto, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga.