Genesis 45:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitamveka kunyumba kwa Farao kuti abale a Yosefe abwera, Faraoyo ndi antchito ake onse adakondwa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mbiri yake inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akunyumba kwa Farao atamva kuti abale ake a Yosefe abwera, Farao pamodzi ndi nduna zake zonse anakondwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mbiri yace inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ace a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ace.