Genesis 45:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono kumeneko akatenge bambo wao ndi mabanja ao, ndipo adzabwere kwa ine kuno. Ndidzaŵapatsa dziko lachonde ku Ejipito kuno, ndipo azidzadya za m'dziko lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Ejipito, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukabwere nawo abambo anu ndi mabanja anu kuno, ndipo ine ndidzakupatsani dera lachonde kwambiri mʼdziko la Igupto. Mudzadya zokoma za mʼdzikoli.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Aigupto, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli.