Genesis 45:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ana a Israele adachitadi zimenezo. Yosefe adaŵapatsa ngolo monga Farao adaalamulira, naŵapatsa phoso lapaulendo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele anachita chotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magaleta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ana a Israeli anachita zimenezo. Yosefe anawapatsa ngolo monga Farao analamulira, ndipo anawapatsanso chakudya cha paulendo wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli anacita cotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magareta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira,