Genesis 45:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bambo wake adamtumizira abulu khumi osenza zipatso zokoma za ku Ejipito, ndi abulu khumi osenza tirigu, buledi ndi zakudya zina za bambo wake zapaulendo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa atate wake anatumiza zotere: abulu khumi osenza zinthu zabwino za m'Ejipito, ndi abulu akazi khumi osenza tirigu, ndi chakudya, ndi phoso la atate la panjira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo abambo ake anawatumizira izi: abulu khumi osenza zinthu zabwino kwambiri za ku Igupto, ndi abulu aakazi khumi osenza tirigu, buledi ndi zakudya zina za pa ulendo wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwa atate wace anatumiza zotere: aburu khumi osenza zinthu zabwino za m'Aigupto, ndi aburu akazi khumi osenza tirigu, ndi cakudya, ndi phoso la atate la panjira.