Genesis 45:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe iwo atamuuza zonse zimene Yosefe adaaŵauza, ndipo iye ataona ngolo zimene Yosefe adaatumiza kuti iye akwerepo popita ku Ejipito, Yakobe adayamba kutsitsimuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magaleta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe atamufotokozera zonse zimene Yosefe anawawuza ndipo ataona ngolo zimene Yosefe anatumiza kuti adzakweremo popita ku Igupto, mtima wa Yakobo, abambo awo unatsitsimuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magareta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka;