Genesis 45:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe adauza abale ake kuti, “Ine ndine Yosefe. Kodi bambo wanga akali moyo?” Koma abale akewo adadzazidwa ndi mantha, kotero kuti sadathenso nkumuyankha komwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Ine ndine Yosefe; kodi akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ake sanakhoze kumyankha iye; pakuti anavutidwa pakumuona iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe anati kwa abale ake, “Ine ndine Yosefe! Kodi abambo anga akanali ndi moyo?” Koma abale ake sanathe kumuyankha chifukwa anali ndi mantha kwambiri pamaso pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anati kwa abale ace, Ine ndine Yosefe; kodi-akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ace sanakhoza kumyankha iye; pakuti anabvutidwa pakumuona iye.