Genesis 45:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsopano musataye mtima kapena kuvutika, popeza kuti Mulungu mwiniwake ndiye amene adanditumiziratu kuno, kuti motero apulumutse moyo wanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsopano musapwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsa ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo tsopano, musawawidwe mtima kapena kudzipsera mtima chifukwa choti munandigulitsa ine kuno, popeza Mulungu ananditsogoza ine kuti adzapulumutse miyoyo yanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsopano musaphwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsira ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo.