Genesis 45:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero sindinu amene mudanditumiza kuno ai, koma Mulungu. Iye wandisandutsa nduna yaikulu ya Farao. Dziko lonse lino lili m'manja mwanga. Ejipito yense ndikulamulira ndine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lake lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Motero, si inu amene munanditumiza kuno koma Mulungu. Iye anandisandutsa kukhala nduna yayikulu ya Farao, ndipo zonse za mʼnyumba mwake zili mʼmanja mwangamu. Komanso amene akulamulira dziko lonse la Igupto ndi ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lace lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Aigupto.