Genesis 45:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano fulumirani, bwererani kwa bambo wanga, mukamuuze kuti mwana wanu Yosefe akunena kuti, ‘Mulungu wandikuza mpaka kukhala wolamulira Ejipito yense, tsono bwerani kuno, musachedwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Fulumirani. Kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Chotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Ejipito lonse: tsikirani kwa ine, musachedwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono fulumirani mubwerere kwa abambo anga ndi kuwawuza kuti, ‘Mwana wanu Yosefe akuti, Mulungu anandisandutsa kukhala mbuye wa dziko lonse la Igupto. Ndiye bwerani kuno musachedwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Fulumirani, kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Cotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Aigupto lonse: tsikirani kwa ine, musacedwe.