Genesis 46:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Israele adasonkhanitsa zake zonse napita ku Beereseba kukapereka nsembe kwa Mulungu wa atate ake Isaki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Israele anamuka ulendo wake ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isaki atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Israeli anasonkhanitsa zonse anali nazo napita ku Beeriseba kukapereka nsembe kwa Mulungu wa abambo ake Isake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Israyeli anamuka ulendo wace ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isake atate wace.