Genesis 46:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
(Asanu ndi aŵiriŵa ndiwo adzukulu a Yakobe amene adabadwa mwa Biliha, amene Labani adaapereka kwa mwana wake Rakele.)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amenewa ndi ana a Biliha, amene Labani anampatsa Rakele mwana wake wamkazi, amenewo anambalira Yakobo; anthu onse ndiwo asanu ndi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amenewa ndi zidzukulu za Yakobo mwa Biliha amene Labani anapereka kwa mwana wake Rakele. Onse pamodzi analipo asanu ndi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amenewa ndi ana a Biliha, amene Labani anampatsa Rakele mwana wace wamkazi, amenewo anambalira Yakobo; anthu onse ndiwo asanu ndi awiri.