Genesis 46:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chiŵerengero chonse cha anthu ochokera mwa Yakobe, amene adapita ku Ejipito, chinali 66, osaŵerengera akazi a ana ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo m'Ejipito, amene anatuluka m'chuuno mwake, pamodzi ndi akazi a ana amuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse amene anapita ndi Yakobo (iwo amene anali akeake, osawerengera akazi a ana ake), analipo 66.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo m'Aigupto, amene anaturuka m'cuuno mwace, pamodzi ndi akazi a ana amuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi;