Genesis 46:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Popeza kuti Yosefe adaabereka ana aŵiri ku Ejipito, chiŵerengero chidafika 70. Onseŵa anali a m'banja la Yakobe, ndipo ndiwo adapita ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi ana amuna a Yosefe, amene anambadwira iye m'Ejipito ndiwo anthu awiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa m'Ejipito anali makumi asanu ndi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pophatikiza ana awiri a Yosefe obadwira ku Igupto, anthu a pa banja la Yakobo amene anapita ku Igupto, onse pamodzi analipo 70.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi ana amuna a Yosefe, amene anambadwira iye m'Aigupto ndiwo anthu awiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa m'Aigupto anali makumi asanu ndi awiri.