Genesis 46:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe adaitanitsa galeta lake, napita ku Goseni kukakumana ndi Israele bambo wake. Atangofika pamaso pake, adamkumbatira m'khosi, nalira nthaŵi yaitali ndithu, osalekerapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe anamanga galeta lake nakwera kunka kukakomana naye Israele atate wake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m'kulira pakhosi pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe anakonza galeta nakwerapo ndi kupita ku Goseni kukakumana ndi abambo ake, Israeli. Yosefe atangofika pamaso pa abambo ake, anawakumbatira nalira kwa nthawi yayitali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anamanga gareta lace nakwera kunka kukakomana naye Israyeli atate wace, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pace nakhala m'kulira pakhosi pace.