Genesis 46:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adamuuza kuti “Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate ako. Usaope kupita ku Ejipito. Kumeneko ndidzachulukitsa zidzukulu zako, kuti zikhale mtundu waukulu wa anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Ejipito; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu. Mulungu wa abambo ako. Usachite mantha kupita ku Igupto, pakuti ndidzachulukitsa zidzukulu zako kumeneko moti zidzakhala mtundu waukulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Aigupto; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukuru;