Genesis 46:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mukamuuze kuti, ‘Ife bwana, ndife oŵeta zoŵeta kuyambira ubwana wathu, monga momwe ankachitira makolo athu.’ Mukatero, ndiye kuti mudzatha kukakhala m'dziko la Goseni.” Yosefe adaanena zimenezi chifukwa choti Aejipito ankanyansidwa ndi abusa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muyankhe kuti, ‘Ife, bwana ndife oweta ziweto kuyambira ubwana wathu mpaka tsopano. Takhala tikuweta ziweto monga mmene ankachitira makolo athu.’ Mukadzayankha choncho, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko la Goseni chifukwa anthu a ku Igupto amanyansidwa nawo anthu oweta ziweto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe ciyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; a cifukwa abusa onse anyansira Aaigupto.