Genesis 47:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yosefe adatenga abale ake asanu napita nawo kwa Farao kukamuuza kuti, “Bambo wanga pamodzi ndi abale anga abwera kuchokera ku Kanani. Abwera ndi zoŵeta zao monga nkhosa ndi ng'ombe, pamodzi ndi zao zonse. Tsopano akukhala m'dziko la Goseni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe analowa nauza Farao nati, Atate wanga ndi abale anga, ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao, ndi zonse ali nazo, anachokera ku dziko la Kanani; ndipo, taonani, ali m'dziko la Goseni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe anapita kukamuwuza Farao kuti, “Abambo anga, abale anga pamodzi ndi nkhosa, ngʼombe zawo, ndi antchito awo abwera kuchokera ku dziko la Kanaani ndipo tsopano ali ku Goseni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe analowa nauza Farao nati, Atate wanga ndi abale anga, ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao, ndi zonse ali nazo, anacokera ku dziko la Kanani; ndipo, taonani, ali m'dziko la Goseni.