Genesis 47:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe adamkhazika m'dziko la Ejipito bambo wake uja, pamodzi ndi abale ake onse aja, ndipo adaŵapatsa malo a nthaka yabwino ndi yachonde, m'chigawo chotchedwa Ramsesi, monga momwe Farao adaalamulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe anakhazika atate wake ndi abale ake, napatsa iwo pokhala m'dziko la Ejipito, m'dera lokometsetsa la m'dziko, m'dziko la Ramsesi, monga analamulira Farao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yosefe anakhazika abambo ake aja ndi abale ake mʼdziko la Igupto. Iye anawapatsa dera la Ramesesi limene linali dziko lachonde kwambiri monga analamulira Farao.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anakhazika atate wace ndi abale ace, napatsa iwo pokhala m'dziko la Aigupto, m'dera lokometsetsa la m'dziko, m'dziko la Ramese, monga analamulira Farao.