Genesis 47:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Njala ija idakula kwambiri, kotero kuti panalibe chakudya pa dziko lonse lapansi, ndipo anthu a ku Ejipito ndi a ku Kanani komwe adafooka nayo njalayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munalibe chakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; chifukwa chake dziko la Ejipito ndi dziko la Kanani tinalefuka chifukwa cha njalayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Njala inakula kwambiri motero kuti chakudya chinasowa mʼdziko lonse. Anthu a ku Igupto ndi ku Kanaani analefuka nayo njalayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munalibe cakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; cifukwa cace dziko la Aaigupto ndi dziko la Kanani unalefuka cifukwa ca njalayo.