Genesis 47:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosefe adasonkhanitsa ndalama zonse zimene anthu a ku Ejipito pamodzi ndi a ku Kanani adaamwaza pogula tirigu. Ndalama zonsezo adazitenga napita nazo kunyumba kwa Farao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama kunyumba ya Farao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse zimene anthu a mu Igupto ndi Kanaani ankapereka pogula tirigu, ndipo anabwera nazo ku nyumba kwa Farao.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m'dziko la Aigupto ndi m'dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama ku nyumba ya Farao.